Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 34:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anakwera kucokera ku zidikha za Moabu, kumka ku phiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Gileadi, kufikira ku Dani;

2. ndi Nafitali lonse, ndi dziko la Efraimu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo;

3. ndi kumwela, ndi cidikha eli cigwa ca Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kufikira ku Zoari.

4. Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 34