Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 33:18-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.

19. Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.

20. Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.

21. Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.

22. Ndi za Dani anati,Dani ndiye mwana wa mkango,Wakutumpha moturuka m'Basana.

23. Za Nafitali anati,Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa,Wodzala ndi mdalitso wa Yehova;Landira kumadzulo ndi kumwela.

24. Ndi za Aseri anati,Aseri adalitsidwe mwa anawo;Akhale wobvomerezeka mwa abale ace,Abviike phazi lace m'mafuta.

25. Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.

26. Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,Wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,Ndi pa mitambo m'ukulu wace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 33