Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 30:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukila mumtima mwanu mwa amitundu onse, amene Yehova Mulungu wanu anakupitikitsiraniko;

2. nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mali ace, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse;

3. pamenepo Yehova Mulungu wanu adzaucotsa ukapolo wanu, ndi kukucitirani cifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.

4. Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;

5. ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala lao lao la makolo anu, nilidzakhala lanu lanu; ndipo adzakucitirani zokoma, ndi kukucurukitsani koposa makolo anu.

6. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.

7. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 30