Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 29:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Awa ndi mau a cipangano cimene Yehova analamulira Mose acicite ndi ana a Israyeli m'dziko la Moabu, pamodzi ndi cipanganoco anacita nao m'Horebe.

2. Ndipo Mose anaitana Israyeli wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anacitira Farao, ndi anyamata ace onse, ndi dziko lace lonse, pamaso panu m'dziko la Aigupto;

3. mayesero akuruwa maso anu anawapenya, zizindikilozo, ndi zozizwa zazikuru zija;

4. koma Yehova sanakupatsani mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.

5. Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'cipululu; zobvala zanu sizinatha pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinatha pa phazi lanu.

6. Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena cakumwa colimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

7. Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, anaturuka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;

8. ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale colowa cao ca Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la hafu la Manase.

9. Cifukwa cace sungani mau a cipangano ici ndi kuwacita, kuti mucite mwanzeru m'zonse muzicita.

10. Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mapfuko anu, akuru anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israyeli;

11. makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 29