Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:42-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zao zao za dzombe.

43. Mlendo wokhala pakati panu adzakulira-kulira inu, koma inu mudzacepera-cepera.

44. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.

45. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;

46. ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.

47. Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi cimwemwe ndi mokondwera mtima, cifukwa ca kucuruka zinthu zonse;

48. cifukwa cace mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lacitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28