Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 26:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. koma Aaigupto anaticitira coipa, natizunza, natisenza nchito yolimba.

7. Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi nchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;

8. ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukuru, ndi zizindikilo, ndi zodabwiza;

9. ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

10. Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kugwadira Yehova Mulungu wanu;

11. ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.

12. Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse caka cacitatu, ndico caka cogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.

13. Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndacotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.

14. Sindinadyako m'cisoni canga, kapena kucotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndacita monga mwa zonse munandilamulira ine.

15. Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israyeli, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

16. Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kucita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwacita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

17. Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zace, ndi kusunga malemba ace, ndi malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi kumvera mau ace.

18. Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu ace ace a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ace onse;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 26