Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israyeli, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.