Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 26:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zocokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mumtanga, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.

3. Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndibvomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.

4. Ndipo wansembe alandire mtanga m'manja mwanu, ndi kuuika pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu.

5. Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye M-aramu wakuti atayike, natsika kumka ku Aigupto, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukuru, wamphamvu, ndi wocuruka anthu ace;

6. koma Aaigupto anaticitira coipa, natizunza, natisenza nchito yolimba.

7. Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi nchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;

8. ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukuru, ndi zizindikilo, ndi zodabwiza;

9. ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

10. Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kugwadira Yehova Mulungu wanu;

11. ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.

12. Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse caka cacitatu, ndico caka cogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.

13. Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndacotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 26