Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 24:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Munthu akatenga mkazi watsopano, asaturuke nayo nkhondo, kapena asamcititse kanthu kali konse; akhale waufulu ku nyumba yace caka cimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.

6. Munthu asalandire cikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo cikole moyo wamunthu.

7. Akampeza munthu waba mbale wace wina wa ana a Israyeli, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzicotsa coipaco pakati panu.

8. Cenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kucita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kucita.

9. Kumbukilani cimene Yehova Mulungu wanu anacitira Miriamu panjira, poturuka inu m'dziko la Aigupto.

10. Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iri yonse, musamalowa m'nyumba mwace kudzitengera cikole cace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 24