Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 24:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pa tsiku lace muzimpatsa kulipira kwace, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wace ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhaireni cimo.

16. Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere cimo lace lace.

17. Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga cikole cobvala ca mkazi wamasiye;

18. koma muzikumbukila kuti munali akapolo m'Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; cifukwa cace ndikuuzani kucita cinthu ici.

19. Mutasenga dzinthuzanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'nchito zonse za manja anu.

20. Mutagwedeza mtengo wanu wa azitona musayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye.

21. Mutachera m'munda wanu wamphesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.

22. Ndipo muzikumbukila kuti munali: akapolo m'dziko la Aigupto; cifukwa cace ndikuuzani kucita cinthu ici.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 24