Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 23:21-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Mukawindira Yehova Mulungu wanu cowinda, musamacedwa kucicita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ici ndithu ndipo mukadacimwako.

22. Koma mukapanda kulonieza cowinda, mulibe kucimwa.

23. Coturuka pa milomo yanu mucisamalire ndi kucicita; monga munaloniezera Yehova Mulungu wanu, copereka caufulu munacilonjeza pakamwa panu.

24. Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni koma musaika kanthu m'cotengera canu.

25. Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi zenga tirigu waciriri wa mnansi wanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 23