Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 23:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mwana wa m'cigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wace wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.

3. M-amoni kapena Mmoabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;

4. popeza sanakukumikani ndi mkate ndi madzi m'njira muja munaturuka m'Aigupto; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesapotamiya, kuti akutemberereni.

5. Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafuna kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.

6. Musawafunira mtendere, kapena cowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.

7. Musamanyansidwa naye M-edomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye M-aigupto, popeza munali alendo m'dziko lace.

8. Ana obadwa nao a mbadwo wacitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.

9. Nkhondo yanu ikaturuka pa adani anu, mudzisunge kusacita coipa ciri conse.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 23