Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 23:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndarama, phindu la cakudya, phindu la kanthu kali konse kokongoletsa.

20. Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.

21. Mukawindira Yehova Mulungu wanu cowinda, musamacedwa kucicita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ici ndithu ndipo mukadacimwako.

22. Koma mukapanda kulonieza cowinda, mulibe kucimwa.

23. Coturuka pa milomo yanu mucisamalire ndi kucicita; monga munaloniezera Yehova Mulungu wanu, copereka caufulu munacilonjeza pakamwa panu.

24. Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni koma musaika kanthu m'cotengera canu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 23