Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 22:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mukapenya buru kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.

5. Mkazi asabvale cobvala ca mwa muna, kapena mwamuna asabvale cobvala ca mkazi; pakuti ali yense wakucita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.

6. Mukacipeza cisa ca mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi mace alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga mace pamodzi ndi ana;

7. muloletu mace amuke, koma mudzitengere ana; kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke.

8. Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lace, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.

9. Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.

10. Musamalima ndi buru ndi ng'ombe zikoke pamodzi.

11. Musamabvala nsaru yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.

12. Mudzipangire mphonje pa ngondya zinai za copfunda canu cimene mudzipfunda naco.

13. Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,

14. namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana nave sindinapeza zizindikilo zakuti ndiye namwali ndithu;

15. pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wace azitenga ndi kuturuka nazo zizindikilo za unamwali wace wa namwaliyo, kumka nazo kwa akuru a mudzi kucipata;

16. ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akuru, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace, koma amuda;

17. ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikilo za unamwali wace in'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikilo za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula cobvalaco pamaso pa akulu a mudziwo.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 22