Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 22:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wace azitenga ndi kuturuka nazo zizindikilo za unamwali wace wa namwaliyo, kumka nazo kwa akuru a mudzi kucipata;

16. ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akuru, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace, koma amuda;

17. ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikilo za unamwali wace in'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikilo za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula cobvalaco pamaso pa akulu a mudziwo.

18. Pamenepo akuru a mudziwo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;

19. ndi kumlipitsa masekeli makumi okha okha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israyeli, ndipo azikhala mkazi wace, sakhoza kumcotsa masiku ace onse.

20. Koma cikakhala coona ici, kuti zizindikilo zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo;

21. pamenepo azimturutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wace, ndipo amuna a mudzi wace azimponya miyala kuti afe; popeza anacita copusa m'Israyeli, kucita cigololo m'nyumba ya atate wace; cotero uzicotsa coipaco pakati panu.

22. Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; cotero muzicotsa coipaco mwa Israyeli.

23. Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona nave;

24. muziwaturutsa onse awiri kumka nao ku cipata ca mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanapfuula angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anacepetsa mkazi wa mnansi wace; cotero muzicotsa coipaco pakati panu.

25. Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;

26. koma namwaliyo musamamcitira kanthu; namwaliyo alibe cimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzace namupha;

27. pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anapfuula, koma panalibe wompulumutsa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 22