Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 20:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.

6. Ndipo ndani munthuyo ananka munda wamphesa osalawa zipatso zace? amuke nabwerere ku nyumba yace, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zace.

7. Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.

8. Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakucita mantha ndi wofumuka mtima? amuke nabwerere kunyumba kwace, ingasungunuke mitima ya abale ace monga mtima wace.

9. Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.

10. Pamene muyandikiza mudzi kucita nao nkhondo, muziupfuulira ndi mtendere.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 20