Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 20:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma za midzi ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale colowa canu, musasiyepo camoyo ciri conse cakupuma;

17. koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;

18. kuti angakuphunzitseni kucita monga mwa zonyansa zao zonse, amazicitira milungu yao; ndipo mungacimwire Yehova Mulungu wanu.

19. Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yace ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?

20. Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wocita nanu nkhondo muumangire macemba, mpaka mukaugonjetsa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 20