Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wocita nanu nkhondo muumangire macemba, mpaka mukaugonjetsa.