Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 20:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene muturuka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magareta ndi anthu akucurukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ali ndi inu.

2. Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,

3. nati nao, Tamverani, Israyeli, muyandikiza kunkhondo lero paadani anu; musalumuka mitima yanu; musacita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;

4. pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.

5. Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 20