Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 2:30-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilola kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wace, nalimbitsa mtima wace, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.

31. Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lace pamaso pako; yamba kulandira dziko lace likhale lako lako.

32. Pamenepo Sihoni anaturuka kukomana nafe, iye ndi anthu ace onse, kugwirana nafe nkhondo ku Yahaza.

33. Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse.

34. Ndipo muja tinalanda midzi yace yonse; ndipo tinaononga konse midzi yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.

35. Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za midzi tidailanda.

36. Kuyambira ku Aroeri, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi ku mudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Gileadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ace; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.

37. Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kuli konse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 2