Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilola kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wace, nalimbitsa mtima wace, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.