Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 19:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Yehova Mulungu wanu ataononga amitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanu lanu, ndi kukhala m'midzi mwao, ndi m'nyumba zao;

2. pamenepo mudzipatulire midzi itatu pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.

3. Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.

4. Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzace wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzace osati dala, osamuda kale lonse;

5. monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzace kutema mitengo, ndi dzanja lace liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguruka m'mpinimo, nikomana ndi mnzace, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;

6. kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzace, pokhala mtima wace watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanaparamula imfa, poona sanamuda kale lonse.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 19