13. Ndipo anthu onse adzamva ndi kucita mantha, osacitanso modzikuza.
14. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanu lanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;
15. mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.
16. Koma asadzicurukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu amke ku Aigupto, kuti acurukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
17. Ndipo asadzicurukitsire akazi, kuti ungapatuke mtinta wace; kapena asadzicurukitsire kwambiri siliva ndi golidi.
18. Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wacifumu wa ufumu wace, adzilemberere cofanana ca cilamuloici m'buku, acitenge pa ici ciri pamaso pa ansembe Alevi;
19. ndipo azikhala naco, nawerengemo masiku onse a moyo wace; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wace, kusunga mau ons acilamulo ici ndi malemba awa, kuwacita;
20. kuti mtima wace usadzikuze pa abaleace, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti acuruke masiku ace, m'ufumu wace, iye ndi ana ace pakati pa Israyeli.