kuti mtima wace usadzikuze pa abaleace, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti acuruke masiku ace, m'ufumu wace, iye ndi ana ace pakati pa Israyeli.