Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 17:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala naco cirema, kapena ciri conse coipa; pakuti cinyansira Yehova Mulungu wanu.

2. Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakucita ciri coipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira cipangano cace,

3. nakatumikira milungu yina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;

4. ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsitsa, ndipo taonani, cikakhala coonadi, coti nzenizeni, conyansaci cacitika m'Israyeli;

5. pamenepo muturutse mwamunayo kapena mkaziyo, anacita coipaco, kumka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.

6. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.

7. Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse, Potero muzicotsa coipaco pakati panu.

8. Ukakulakani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo mirandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kumka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

9. nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ace.

10. Ndipo mucite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kucita monga mwa zonse akulangizanizi,

11. Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa ciweruzo akufotokozerani, mucite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.

12. Koma munthu wakucita modzikuza, osamvera wansembe wokhala ciriri kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo mucotse coipaco kwa Israyeli.

13. Ndipo anthu onse adzamva ndi kucita mantha, osacitanso modzikuza.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 17