Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 14:16-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. ndi nkhutukutu, ndi mancici, ndi tsekwe;

17. ndi bvuwo, ndi dembu, ndi nswankhono;

18. ndi iodwa, ndi cimeza, monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.

19. Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.

20. Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.

21. Musamadya cinthu ciri conse citafa cokha; muzipereka ico kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, acidye ndiye; kapena ucigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.

22. Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, caka ndi caka.

23. Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo iye, kukhalitsamo dzina lace; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.

24. Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lace, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;

25. pamenepo mulisinthe ndarama, ndi kumanga ndarama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 14