Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 13:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukucetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba va akapolo.

11. Kuti Israyeli wonse amve, ndi kuopa, ndi kusaonieza kucita coipa cotere conga ici pakati pa inu.

12. Ukamva za umodzi wa midzi yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,

13. Amuna ena opanda pace anaturuka pakati pa inu, naceta okhala m'mudzi mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu yina, imene simunaidziwa;

14. pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, cikakhala coona, catsimikizika cinthuci, kuti conyansa cotere cacitika pakati pa inu;

15. muzikanthatu okhala m'mudzi muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuuononga konse, ndi zonse ziri m'mwemo, ng'ombe zace zomwe, ndi lupanga lakuthwa.

16. Ndipo muzikundika zofunkha zace zonse pakati pakhwalala pace, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zace zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.

17. Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka cinthu coti cionongeke; kuti Yehova a aleke mkwiyo wacewaukali, nakucitireni cifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukucurukitsani monga analumbirira makolo anu;

18. pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace onse amene ndikuuzani lero lino, kucita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 13