Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. ndi kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

10. Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Aigupto lija mudaturukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;

11. koma dziko limene mumkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;

12. ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo cikhalire, kuyambira caka mpaka kutsiriza caka.

13. Ndipo kudzakhala mukasamalira cisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,

14. ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yace, ya myundo ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11