Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Cifukwa cace muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m'moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati cizindikilo pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu.

19. Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.

20. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu;

21. kuti masiku anu ndi masiku a ana anu acuruke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo liri pamwamba pa dziko.

22. Pakuti mukasunga cisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwacita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace zonse, ndi kummamatira;

23. Yehova adzapitikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu akuru ndi amphamvu oposa inu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11