Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, a nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zace; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.

18. Cifukwa cace muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m'moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati cizindikilo pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu.

19. Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.

20. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu;

21. kuti masiku anu ndi masiku a ana anu acuruke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo liri pamwamba pa dziko.

22. Pakuti mukasunga cisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwacita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace zonse, ndi kummamatira;

23. Yehova adzapitikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu akuru ndi amphamvu oposa inu.

24. Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira cipululu ndi Lebano, kuyambira nyanjayo, nyanja ya Pirate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malice anu.

25. Palibe munthu adzaima paraaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, cifukwa ca inu, monga ananena ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11