Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 9:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka coyamba ca Dariyo mwana wa Ahaswero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Akasidi;

2. caka coyamba ca ufumu wace, ine Danieli ndinazindikira mwa mabuku kuti ciwerengo cace ca zaka, cimene mau a Yehova anadzera naco kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.

3. Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.

4. Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kubvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi cifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,

5. tacimwa, tacita mphulupulu, tacita zoipa, tapanduka, kupambuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;

6. sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.

7. Ambuye, cilungamo nca Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisrayeli onse okhala pafupi ndi okhala kutali, ku maiko onse kumene mudawaingira, cifukwa ca kulakwa kwao anakulakwirani nako.

Werengani mutu wathunthu Danieli 9