Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 8:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabrieli, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.

17. Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinacita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya cimariziro.

18. Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikuru, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo,

19. Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa cimene cidzacitika pa citsiriziro ca mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pace,

20. Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya.

21. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene, ndi nyanga yaikuru iri pakati pa maso ace ndiyo mfumu yoyamba.

22. Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwace mwa iyo itatyoka, adzauka maufumu anai ocokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.

23. Ndipo potsiriza pace pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.

24. Ndi mphamvu yace idzakhala yaikuru, koma si mphamvu yace yace ai, nidzaononga modabwiza, nidzakuzika, ndi kucita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.

25. Ndipo mwa kucenjera kwace adzapindulitsa cinyengo m'dzanja mwace, nadzadzikuza m'mtima mwace; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzatyoledwa popanda dzanja.

26. Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzacitika atapita masiku ambiri.

27. Ndipo ine Danieli ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kucita nchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.

Werengani mutu wathunthu Danieli 8