Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 7:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo ndinapenyera cifukwa ca phokoso la mau akuru idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adacipha ciromboci, ndi kuononga mtembo wace, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.

12. Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.

13. Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.

14. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.

15. Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.

16. Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:

17. Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.

18. Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.

Werengani mutu wathunthu Danieli 7