Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 5:16-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.

17. Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.

18. Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi cifumu;

19. ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.

20. Koma pokwezeka mtima wace, nulimba mzimu wace kucita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wace, namcotsera ulemerero wace;

21. ndipo anamuinga kumcotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wace unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pace mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira ali yense Iye afuna mwini.

22. Ndipo inu mwana wace, Belisazara inu, simunadzicepetsa m'mtima mwanu, cinkana munazidziwa izi zonse;

23. koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yace kwa inu; ndi inu ndi akuru anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolidi, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona, kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwace muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamcitira ulemu.

24. Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kucokera pamaso pace, nililembedwa lembali.

25. Ndipolembalolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UF ARSIN.

26. Kumasulira kwace kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.

27. TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera.

28. PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.

Werengani mutu wathunthu Danieli 5