Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 3:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. ndipo ali yense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

7. Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi zoyimbitsa ziri zonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolidi adaliimika mfumu Nebukadinezara.

8. Cifukwa cace anayandikira Akasidi ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda.

9. Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.

10. Inu mfumu mwalamulira kuti munthu ali yense amene adzamva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, agwadire, nalambire fanolo lagolidi;

11. ndi yense wosagwadira ndi kulambiraadzaponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

12. Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire nchito ya dera la ku Babulo, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amuna awa, mfumu, sanasamalira inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

13. Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wace, anawauza abwere nao Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

14. Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolidi ndinaliimikalo?

15. Mukabvomereza tsono, pakumva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, cabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?

16. Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.

17. Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

18. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

Werengani mutu wathunthu Danieli 3