Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:41-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zace, mwina dongo la woumba, mwina citsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya citsulo; popeza mudaona citsulo cosanganizika ndi dongo.

42. Ndi zala za mapazi, mwina citsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka.

43. Ndi umo mudaonera citsulo cosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzapharikizana, monga umo citsulo sicimasanganizikana ndi dongo.

44. Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzao nongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wace sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse nudzakhala cikhalire.

45. Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera citsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golidi; Mulungu wamkuru wadziwitsa mfumu cidzacitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwace kwakhazikika.

46. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yace pansi, nalambira Danieli, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.

47. Mfumu inamyankha Danieli, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wobvumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kubvumbulutsa cinsinsi ici.

48. Pamenepo mfumu inasandutsa Danieli wamkuru, nimpatsa mphatso zazikuru zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babulo; nakhala iye kazembe wamkuru wa anzeru onse a ku Babulo.

Werengani mutu wathunthu Danieli 2