Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:30-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Koma ine, cinsinsi ici sicinabvumbulutsidwa kwa ine cifukwa ca nzeru ndiri nayo yakuposa wina ali yense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.

31. Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikuru. Fanoli linali lalikuru, ndi kunyezimira kwace kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ace anali oopsa,

32. Pano ili tsono, mutu wace unali wagolidi wabwino, cifuwa cace ndi manja ace zasiliva, mimba yace ndi cuuno cace zamkuwa,

33. miyendo yace yacitsulo, mapazi ace mwina citsulo mwina dongo.

34. Munali cipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ace okhala citsulo ndi dongo, nuwaphwanya.

35. Pamenepo citsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikuru, nudzaza dziko lonse lapansi.

Werengani mutu wathunthu Danieli 2