Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 12:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndinacimva ici, koma osacizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, citsiriziro ca izi nciani?

9. Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa cizindikilo mpaka nthawi ya citsiriziro.

10. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzacita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.

11. Ndipo kuyambira nthawi yoti idzacotsedwa nsembe yacikhalire, nicidzaimika conyansa cakupululutsa, adzakhalanso masiku cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

12. Wodala iye amene ayembekeza, nafikira ku masiku cikwi cimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.

13. Koma iwe, muka mpaka cimariziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.

Werengani mutu wathunthu Danieli 12