Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 11:20-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo m'malo mwace adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzatyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai.

21. Ndi m'malo mwace adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatsa ulemu wa ufumu, koma adzafika kacetecete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

22. Ndipo mwa mayendedwe ace a cigumula adzakokololedwa pamaso pace, nadzatyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa cipangano.

23. Ndipo atapangana naye adzacita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.

24. Adzafika kacetecete ku minda yokometsetsa ya derali, nadzacita cosacita atate ace, kapena makolo ace; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi cuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zace; adzatero nthawi.

25. Nadzautsa mphamvu yace ndi mtima wace ayambane ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru la nkhondo; ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.

26. Inde iwo akudyako cakudya cace adzamuononga; ndi ankhondo ace adzasefukira, nadzagwaambiri ophedwa.

27. Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kucita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwace kudzakhala pa nthawi yoikika.

28. Ndipo adzabwerera ku dziko lace ndi cuma cambiri; ndi mtima wace udzatsutsana ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace, ndi kubwerera ku dziko lace.

29. Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwela; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.

30. Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; cifukwa cace adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace; adzabweranso, nadzasamalira otaya cipangano copatulika.

31. Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lace; nadzacotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa conyansa copululutsaco.

32. Ndipo akucitira coipa cipanganoco iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzacita mwamphamvu.

33. Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.

34. Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.

35. Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya citsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.

Werengani mutu wathunthu Danieli 11