Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 8:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.

10. Ndipo ndidzasanduliza madyerero anu, akhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'cuuno monse, ndi mpala pa mutu uli wonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi citsiriziro cace ngati tsiku lowawa.

11. Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m'dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mau a Yehova.

12. Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.

13. Tsiku lomwelo anamwali okongola ndi anyamata adzakomoka nalo ludzu.

14. Iwo akulumbira ndi kuchula cimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.

Werengani mutu wathunthu Amosi 8