Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 3:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Bukitsani ku nyumba zacifumu za Asidodi, ndi ku nyumba zacifumu za m'dziko la Aigupto, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akuru m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwace.

10. Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.

11. Cifukwa cace, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pace pa dziko, nadzatsitsa kukucotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zacifumu adzazifunkha.

12. Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israyeli okhala pansi m'Samariya, m'ngondya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.

13. Tamverani inu, mucitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Amosi 3