Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israyeli okhala pansi m'Samariya, m'ngondya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.