Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 3:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.

11. Cifukwa cace, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pace pa dziko, nadzatsitsa kukucotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zacifumu adzazifunkha.

12. Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israyeli okhala pansi m'Samariya, m'ngondya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.

13. Tamverani inu, mucitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu.

14. Pakuti tsiku lakumlanga Israyeli cifukwa ca zolakwa zace, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Beteli; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.

15. Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yacisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuruzo zidzatha, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Amosi 3