Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 1 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Cilango ca Mulungu pa amitundu ozinga Israyeli

1. MAU a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekoa, ndiwo amene anawaona za Israyeli masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli, zitatsala zaka ziwiri cisanafike cibvomezi.

2. Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ace ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzacita cisoni, ndi mutu wa Karimeli udzauma.

3. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapuntha Gileadi ndi zopunthira zacitsulo;

4. koma ndidzatumiza moto ku nyumba ya Hazaeli, ndipo udzanyeketsa nyumba zacifumu za Benihadadi.

5. Ndipo ndidzatyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'cigwa ca Aveni, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.

6. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;

7. koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zace zacifumu;

8. ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.

9. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Turo, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukila pangano lacibale;

10. koma ndidzatumiza moto pa linga la Turo, ndipo udzanyeketsa nyumba zace zacifumu.

11. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza analondola mphwace ndi lupanga, nafetsa cifundo cace conse, ndi mkwiyo wace unang'amba cing'ambire, nasunga mkwiyo wace cisungire;

12. koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Bozira.

13. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Gileadi, kuti akuze malire ao;

14. koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zacifumu zace, ndi kupfuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kabvumvulu;

15. ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ace pamodzi, ati Yehova.