Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 8:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo m'tsogolo mwace Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa; Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.

2. Ndipo anakantha Amoabu nawayesa ndi cingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi cingwe cimodzi cathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera: nayo mitulo.

3. Davide anakanthanso Hadadezeri, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wace ku cimtsinje ca Firate.

4. Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.

5. Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

6. Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko, Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kuli konse anamukako.

7. Ndipo Davide anatenga zikopa zagolidi zinali ndi anyamata a Hadadezeri, nabwera nazo ku Yerusalemu.

8. Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezeri, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 8