Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 6:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo kunali pamene likasa la Yehova tinafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikubvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwace.

17. Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analgka pamalo pace pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

18. Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu.

19. Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israyeli, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa, Ndipo anthu aja onse anabwera yense ku nyumba yace.

20. Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yace. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anaturukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israyeli inalemekezeka ndithu, amene anabvula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ace, monga munthu woluluka abvula wopanda manyazi!

21. Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lace lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israyeli, cifukwa cace ndidzasewera pamaso pa Yehova.

22. Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzicepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.

23. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli sanaona mwana kufikira tsiku la imfa yace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 6