Ndipo kunali pamene likasa la Yehova tinafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikubvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwace.