Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:25-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Mumdziwa Abineri mwana wa Neri kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kuturuka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikucita inu.

26. Ndipo Yoabu anaturuka kwa Davide, natumizira Abineri mithenga, amene anambweza ku citsime ca Sira. Koma Davide sanacidziwa.

27. Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.

28. Ndipo pambuyo pace, pakucimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osacimwira mwazi wa Abineri mwana wa Neri, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;

29. cilango cigwere pa mutu wa Yoabu ndi pa nyumba yonse ya atate wace; ndipo kusasoweke ku nyumba ya Yoabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa cakudya.

30. Motero Yoabu ndi Abisai mbale wace adapha Abineri, popeza iye adapha mbale wao Asaheli ku Gibeoni, kunkhondo.

31. Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zobvala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'cuuno, nimulire Abineri. Ndipo mfumu Davide anatsata cithatha.

32. Ndipo anaika Abineri ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ace nilira ku manda a Abineri, nalira anthu onse.

33. Ndipo mfumu inanenera Abineri nyimbo iyi ya maliro, niti,Kodi Abineri anayenera kufa ngati citsiru?

34. Manja anu sanamangidwa, mapazi anu sanalongedwa m'zigologolo;Monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu.Ndipo anthu onse anamliranso.

35. Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide cakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.

36. Ndipo anthu onse anacisamalira, ndipo cinawakomera; ziri zonse adazicita mfumu zidakomera anthu onse.

37. Momwemo anthu onse ndi Aisrayeli onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumira kwa mfumu kupha Abineri mwana wa Neri.

38. Ndipo mfumu inati kwa anyamata ace, Simudziwa kodi kuti kalonga, ndi munthu womveka, wagwa lero m'Israyeli?

39. Ndipo ndikali wofoka ine lero, cinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wocita coipa monga mwa coipa cace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3