Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba cilimbire, ndi nyumba ya Sauli inafoka cifokere.

2. Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Amnoni, wa Ahinoamu wa ku Jezreeli;

3. waciwiri Kileabu, wa Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli; ndi wacitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;

4. ndi wacinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wacisanu Sefatiya mwana wa Abitali;

5. ndi wacisanu ndi cimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni.

6. Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide, Abineri analimbikira nyumba ya Sauli.

7. Ndipo Sauli adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lace ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga?

8. Pomwepo Abineri anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa gam wa Yuda kodi? Lero lino ndirikucitira zokoma nyumba ya Sauli atate wanu, ndi abale ace, ndi abwenzi ace, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.

9. Mulungu alange Abineri, naonjezepo, ndikapanda kumcitira Davide monga Yehova anamlumbirira;

10. kucotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazika mpando wadfumu wa Davide pa Israyeli ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

11. Ndipo iye sanakhoza kuyankha Abineri mau amodzi cifukwa ca kumuopa iye.

12. Ndipo Abineri anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisrayeli onse atsate inu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3