Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 23:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Josebu-basebete Mtakemoni, mkuru wa akazembe; ameneyu ndiye Adino M-ezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9. Ndipo wotsatana naye Eleazeri mwana wa Dodai mwana wa M-akohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atacoka Aisrayeli;

10. iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lace linalema, ndi dzanja lace lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwace kukafunkha kokha.

11. Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Mharario Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12. Koma iyeyoanaima pakati pa mundawo, naucinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru.

13. Ndipo atatu a mwamakumi atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti Gnamanga zithando m'cigwa ca Refaimu.

14. Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu.

15. Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! wina akadandipatsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri pacipatapo!

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 23